September 7, 2024
Nkhotakota, Malawi
National

A Dalitso Kabambe alowa mchipani cha UTM

A Dalitso Kabambe, omwe adalengeza posachedwapa kuti atuluka mchipani cha Democratic Progressive (DPP), alowa mchipani cha United Transformation Movement (UTM).
A Kabambe alandiridwa lero m’boma la Thyolo.
Mukulankhula kwake, Kabambe wati iwo achita izi malingana ndi ufulu omwe malamulo a dziko lino amapeleka kwa mzika za dziko lino kukhala kapena kusakhala limodzi pa gulu la anthu.
Iye wati wakhala akuwelenga mfundo ndi malamulo a zipani zochuluka mdziko muno koma mfundo zomwe zinawagwira mtima zinali za chipani cha UTM.
Pamwambowu, pali mlembi wa mkulu wa chipani cha UTM, Patricia Kaliat, mneneri wa chipanichi Felix Njawala ndi akuluakulu ena mchipanichi.